Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 6:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo a ocita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire cisomo ca Mulungu kwacabe inu,

2. (pakuti anena,M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe,Ndipo m'tsiku la cipulumutso ndinakuthandiza;Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la cipulumutso);

3. osapatsa cokhumudwitsa konse m'cinthu ciri conse, kuti utumikiwo usanenezedwe;

4. koma m'zonse tidzitsimikfzira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,

5. m'mikwingwirima, m'ndende, m'mapokoso, m'mabvutitso, m'madikiro, m'masalo a cakudya;

6. m'mayeredwe, m'cidziwitso, m'cilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'cikondi cosanyenga;

7. m'mau a coonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa camuna ca cilungamo kulamanja ndi kulamanzere,

8. mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; mongaosoceretsa, angakhale ali oona;

9. monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani, tiri ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;

10. monga akumva cisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, lroma akulemeretsa ambiri; mensa okhala opanda-kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.

11. M'kamwa mwathu mmotseguka kwa inu Akorinto, mtima wathu wakulitsidwa.

12. Simupsinjika mwa ife, koma mupsiniika mumtima mwanu.

13. Ndipo kukhale cibwezero comweci (ndinena monga ndi ana anga) mukulitsidwe inunso.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 6