1. Ndipo a ocita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire cisomo ca Mulungu kwacabe inu,
2. (pakuti anena,M'nyengo yolandiridwa ndinamva iwe,Ndipo m'tsiku la cipulumutso ndinakuthandiza;Taonani, tsopano ndiyo nyengo yabwino yolandiridwa, taonani, tsopano ndilo tsiku la cipulumutso);
3. osapatsa cokhumudwitsa konse m'cinthu ciri conse, kuti utumikiwo usanenezedwe;
4. koma m'zonse tidzitsimikfzira ife tokha monga atumiki a Mulungu, m'kupirira kwambiri, m'zisautso, m'zikakamizo, m'zopsinja,
5. m'mikwingwirima, m'ndende, m'mapokoso, m'mabvutitso, m'madikiro, m'masalo a cakudya;
6. m'mayeredwe, m'cidziwitso, m'cilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'cikondi cosanyenga;
7. m'mau a coonadi, mu mphamvu ya Mulungu; mwa camuna ca cilungamo kulamanja ndi kulamanzere,
8. mwa ulemerero, mwa mnyozo, mwa mbiri yoipa ndi mbiri yabwino; mongaosoceretsa, angakhale ali oona;
9. monga osadziwika, angakhale adziwika bwino; monga alinkufa, ndipo taonani, tiri ndi moyo; monga olangika, ndipo osaphedwa;
10. monga akumva cisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, lroma akulemeretsa ambiri; mensa okhala opanda-kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.