Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 5:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pakuti cikondi ca Kristu citikakamiza; popeza taweruza cotero, kuti mmodzi adafera onse, cifukwa cace onse adafa;

15. ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyoasakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo, nauka.

16. Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Kristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.

17. Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano,

18. Koma zinthu zonse zicokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa iye yekha mwa Kristu, natipatsa utumiki wa ciyanjanitso;

19. ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Kristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iyeyekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a ciyanjanitso,

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 5