Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 5:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Sitidzibvomeretsanso ife tokha kwa inu, koma tikupatsani inu cifukwa ca kudzitamandira pa ife, kuti mukakhale nako kanthu kakutsutsana nao iwo akudzitamandira pooneka pokha, osati mumtima.

13. Pakuti ngati tiri oyaruka, titero kwa Mulungu; ngati tiri a nzeru zathu, titero kwa inu.

14. Pakuti cikondi ca Kristu citikakamiza; popeza taweruza cotero, kuti mmodzi adafera onse, cifukwa cace onse adafa;

15. ndipo adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyoasakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo, nauka.

16. Kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi; ndipo ngati tazindikira Kristu monga mwa thupi, koma tsopano sitimzindikiranso motero.

17. Cifukwa cace ngati munthu ali yense ali mwa Kristu ali wolengedwa watsopano; zinthu zakale zapita, taonani, zakhala zatsopano,

18. Koma zinthu zonse zicokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa iye yekha mwa Kristu, natipatsa utumiki wa ciyanjanitso;

19. ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Kristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iyeyekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a ciyanjanitso,

20. Cifukwa cace tiri atumiki m'malo mwa Kristu, monga ngati Mulungu alikudandaulira mwa ife; tiumiriza inu m'malo mwa Kristu, yanjanitsidwani ndi Mulungu,

21. Ameneyo sanadziwa ucimo anamyesera ucimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale cilungamo ca Mulungu mwa iye.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 5