Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 2:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Koma amene mumkhululukira kanthu, inenso nditero naye; pakuti cimene ndakhululukira inenso, ngati ndakhululukira kanthu, ndacicita cifukwa ca inu, pamasopa Kristu;

11. kuti asaticenierere Satana; pakuti sitikhala osadziwa macenjerero ace.

12. Koma pamene ndinadza ku Trowa kudzalalikira Uthenga Wabwino wa Kristu, ndipo pamene padanditsegukira kwa ine pakhomo, mwa Ambuye,

13. ndinalibe mpumulo mu mzimu wanga, posapeza ine Tito mbale wanga; koma polawirana nao ndinanka ku Makedoniya.

14. Koma ayamikike Mulungu, amene atitsogolera m'cigonjetso mwa Kristu, namveketsa pfungo la cidziwitso cace mwa ife pamalo ponse.

15. Pakuti ife ndife pfungo labwino la Kristu, kwa Mulungu, mwa iwo akupulumutsidwa, ndi mwa iwo akuonongeka; kwa ena pfungo la imfa kuimfa;

16. koma kwa ena pfungo la moyo kumoyo. Ndipo azikwanira ndani izi?

17. Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akucita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa coona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 2