Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 2:1-4 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma ndinatsimikiza mtima mwa ine ndekha, ndisadzenso kwa inu ndi cisoni.

2. Pakuti ngati ine ndimvetsa inu cisoni, ndaninso amene adzandikondweretsa ine, kama iye amene ndammvetsa cisoni?

3. Ndipo ndinalemba ici comwe, kuti pakudza ndisakhale naco cisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti cimwemwe canga ndi canu ca inu nonse.

4. Pakuti m'cisautso cambiri ndi kuwawa mtima ndinalembera inu ndi misozi yambiri; si kuti ndikumvetseni cisoni, koma kuti mukadziwe cikondi ca kwa inu, cimene ndiri naco koposa.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 2