Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 12:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndiyenera kudzitamandira, kungakhale sikupindulika; koma ndidzadza ku masomphenya ndi mabvumbulutso a Ambuye.

2. Ndidziwa munthu wa mwa Kristu, zitapita zaka khumi ndi zinai (ngati m'thupi, sindidziwa; ngati kunja kwa thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu), anakwatulidwa wotereyo kunka naye Kumwamba kwacitatu.

3. Ndipo ndidziwa munthu wotereyo (ngati m'thupi, ngati wopanda thupi, sindidziwa; adziwa Mulungu),

4. kuti anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka, amene saloleka kwa munthu kulankhula.

5. Cifukwa ca wotereyo ndidzadzitamandira; koma cifukwa ca Ine ndekha sindidzadzitamandira, koma m'zofoka zanga,

6. Pakuti ngati ndikafuna kudzitamandira, sindidzakhala wopanda nzeru; pakuti ndidzanena coonadi; koma ndileka, kuti wina angandiwerengere ine koposa kumene andiona ine, kapena amva za ine.

7. Ndipo kuti ndingakwezeke koposa, cifukwa ca ukulu woposa wa mabvumbulutso, kunapatsidwa kwa ine munga m'thupi, ndiye mngelowa Satana kutianditundudze, kuti ndingakwezeke koposa.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 12