Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 11:5-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Pakuti ndiyesa kuti sindinaperewera konse ndi atumwi oposatu,

6. Ndipo ndingakhale ndiri wosaphunzira m'manenedwe, koma sinditero m'cidziwitso, koma m'zonse tacionetsa kwa inu mwa anthu onse.

7. Kodi ndacimwa podzicepetsa ndekha, kuti inu mukakwezedwe, popeza ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu?

8. ndinalanda za Mipingo yina, ndi kulandira kwa iwo kulipira kuti ndikatumikire inu;

9. ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitsa munthu ali yense; pakuti abale akucokera ku Makedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinacenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzacenjerapo.

10. Coonadi ca Kristu ciri mwa ine, kuti kudzitamandira kumene sikudzaletsedwa kwa ine mu mbali za Akaya,

11. Cifukwa ninji? Cifukwa sindikonda inu kodi? Adziwa Mulungu.

12. Koma cimene ndicita, ndidzacitanso, kuti ndikawadulire cifukwa iwo akufuna cifukwa; kuti m'mene adzitamandiramo, apezedwe monganso ife.

13. Pakuti otere ali atumwi onyenga, ocita ocenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Kristu,

14. Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.

15. Cifukwa cace sikuli kanthu kwakukuru ngatinso atumiki ace adzionetsa monga atumiki a cilungamo; amene cimariziro cao cidzakhala monga nchito zao.

16. Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang'ono.

17. Cimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.

18. Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 11