Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 11:19-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha.

20. Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.

21. Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofoka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.

22. Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali Aisrayeli? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso.

23. Kodi ali atumiki a Kristu? (ndilankhula monga moyaruka), makamaka ine; m'zibvutitso mocurukira, m'ndende mocurukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawiri kawiri.

24. Kwa Ayuda ndinalandirakasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.

25. Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka combo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;

26. paulendo kawiri kawiri, moopsya mwace mwa mitsinje, moopsya mwace mwa olanda, 1 moopsya modzera kwa mtundu wanga, moopsya modzera kwa amitundu, moopsya m'mudzi, moopsya m'cipululu, moopsya m'nyanja, moopsya mwaabale onyenga;

27. m'cibvutitso ndi m'colemetsa, m'madikiro kawiri kawiri, 2 m'njala ndi ludzu, m'masalo a cakudyakawiri kawiri, m'cisanu ndi umarisece.

28. Popanda zakunjazo pali condisindikiza tsiku ndi tsiku, calabadiro ca Mipingo yonse.

29. 3 Afoka ndani wosafoka inenso? Akhumudwitsidwa ndani, wosatenthanso ine?

30. Ngati ndiyenerakudzitamandira, 4 ndidzadzitamandira ndi za kufoka kwanga.

31. Mulungu Atate wa Ambuye Yesu, iye amene alemekezeka ku nthawi yonse, adziwa kuti sindinama.

32. M'Damasiko kazembe wa mfumu Areta analindizitsa mudzi wa Adamasiko kuti andigwire ine;

33. ndipo mwa zenera, mumtanga, ananditsitsa pakhoma, ndipo ndinapulumuka m'manja mwace.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 11