Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 11:16-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Ndinenanso, Munthu asandiyese wopanda nzeru; koma ngati mutero, mundilandirenso ine monga wopanda nzeru, kuti inenso ndidzitamandire pang'ono.

17. Cimene ndilankhula sindilankhula monga mwa Ambuye, koma monga wopanda nzeru, m'kulimbika kumene kwa kudzitamandira.

18. Popeza ambiri adzitamandira monga mwa thupi, inenso ndidzadzitamandira.

19. Pakuti mulolana nao opanda nzeru mokondwera, pokhala anzeru inu nokha.

20. Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.

21. Ndinena monga mwa kunyoza, monga ngati tinakhala ofoka. Koma m'mene wina alimbika mtimamo (ndinena mopanda nzeru) momwemo ndilimbika mtima inenso.

22. Kodi ali Ahebri? Inenso. Kodi ali Aisrayeli? Inenso. Kodi ali mbeu ya Abrahamu? Inenso.

23. Kodi ali atumiki a Kristu? (ndilankhula monga moyaruka), makamaka ine; m'zibvutitso mocurukira, m'ndende mocurukira, m'mikwingwirima mosawerengeka, muimfa kawiri kawiri.

24. Kwa Ayuda ndinalandirakasanu mikwingwirima makumi anai kuperewera umodzi.

25. Katatu ndinamenyedwa ndi ndodo, kamodzi ndinaponyedwa miyala, katatu ndinatayika posweka combo, ndinakhala m'kuya tsiku limodzi usana ndi usiku;

26. paulendo kawiri kawiri, moopsya mwace mwa mitsinje, moopsya mwace mwa olanda, 1 moopsya modzera kwa mtundu wanga, moopsya modzera kwa amitundu, moopsya m'mudzi, moopsya m'cipululu, moopsya m'nyanja, moopsya mwaabale onyenga;

27. m'cibvutitso ndi m'colemetsa, m'madikiro kawiri kawiri, 2 m'njala ndi ludzu, m'masalo a cakudyakawiri kawiri, m'cisanu ndi umarisece.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 11