Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 10:15-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

15. osadzitamandira popitirira muyeso mwa macititso a ena; koma tiri naco ciyembekezo kuti pakukula cikhulupiriro canu, tidzakulitsidwa mwa inu monga mwa cilekezero cathu kwa kucurukira,

16. kukalalikira Uthenga Wabwino m'tsogolo mwace mwa inu, sikudzitamandira mwa cilekezero ca wina, ndi zinthu zokonzeka kale.

17. Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye;

18. pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wobvomerezeka.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 10