Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Akorinto 1:9-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. koma tokha tinakhala naco citsutso ca imfa mwa ife tokha, kuti tisalimbike pa ife tokha, koma pa Mulungu wakuukitsa akufa;

10. amene anatilanditsa mu imfa yaikuru yotere, nadzalanditsa;

11. amene timyembekezera kuti adzalanditsanso; pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri cifukwa ca ife.

12. Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa cikumbu mtima cathu, kuti m'ciyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'cisomo ca Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.

Werengani mutu wathunthu 2 Akorinto 1