Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Yohane 5:9-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Ngati tilandira umboni wa anthu, umboni wa Mulungu uposa; cifukwa umboni wa Mulungu ndi uwu, kuti anacita umboni za Mwana wace.

10. Iye amene amkhulupirira Mwana wa Mulungu ali nao umboni mwa iye; ye wosakhulupirira Mulungu ananuyesa iye wonama; cifukwa sanakhulupirira umboni wa Mulungu anaucita wa Mwana wace.

11. Ndipo uwu ndi umboniwo, kuti Mulungu anatipatsa ife moyo wosatha, ndipo moyo umene uli mwa Mwana wace.

12. Iye wakukhala ndi Mwana ali nao moyo; wosakhala ndi Mwana wa Mulungu alibe moyo.

13. Izi ndakulemberani, kuti mudziwe kuti muli ndi moyo wosatha, inu amene mukhulupirira dzina la Mwana wa Mulungu.

14. Ndipo uku ndi kulimbika mrima kumene tiri nako kwa iye, kuti ngati tipempha kanthu monga mwa cifuniro cace, atimvera;

15. ndipo ngati tidziwa kuti atimvera ciri conse ticipempha, tidziwa kuti tiri nazo izi tazipempha kwa iye.

Werengani mutu wathunthu 1 Yohane 5