Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 5:7-22 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Ndipo izi ulamulire, kuti akhale opanda ciremao

8. Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yace ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lace, wakana cikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.

9. Asawerengedwe wamasiye ngati sanafikire zaka makumi asanu ndi limodzi, atakhala mkazi wa mwamuna mmodzi,

10. wa mbiri ya nchito zabwino; ngati walera ana, ngati wacereza alendo, ngati adasambitsa mapazi a nzera mtima, ngati wathapdiza osautsidwa, ngati anatsatadi nchito zonse zabwino.

11. Koma amasiyeang'ono uwakane; pakuti pamene ayambakumcitira Kristu cipongwe afuna kukwatiwa;

12. pokhala naco citsutso, popeza adataya cikhulupiriro cao coyamba.

13. Ndipo aphunziraponso kucita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pace, nacita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.

14. Cifukwa cace nditi akwatiwe amasiye ang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa cifukwa kwa mdaniyo cakulalatira;

15. pakuti adayamba enakupatuka ndi kutsata Satana.

16. Ngati mkazi wina wokhulupira ali nao amasiye, iye awathandize, ndipo Mpingowo usalemedwe; kuti uthandize iwo amene ali amasiye ndithu.

17. Akuru akuweruza bwino ayesedwe oyenera ulemu wowirikiza, makamaka iwo akucititsa m'mau ndi m'ciphunzitso.

18. Pakuti malembo ati, Usapunamiza ng'ombe yopuntha tirigu. Ndipo, Wogwira nchito ayenera kulipira kwace.

19. Pa mkulu usalandire comnenera, koma pakhale mboni ziwiri kapena zitatu.

20. Iwo akucimwa uwadzudzule pamaso pa onse, kuti otsalawo acite mantha.

21. Ndikucitira umboni pamaso pa Mulungu, ndi Kristu Yesu, ndi angelo osankhika, kuti usunge izi kopanda kusankhiratu, wosacita kanthu monga mwa tsankhu.

22. Usafulumira kuika manja pa munthu ali yense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 5