Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 5:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mkulu usamdzudzule, komatu umdandaulire ngati atate; anyamata ngati abale;

2. akazi akulu ngati amai; akazi ang'ono ngati alongo, m'kuyera mtima konse.

3. Citira ulemu amasiye amene ali amasiye ndithu.

4. Koma ngati wamasiye wina ali nao ana kapena adzukulu, ayambe aphunzire iwo kucitira ulemu a m'banja lao, ndi kubwezera akuwabala; pakuti ici ncolandirika pamaso pa Mulungu.

5. Koma iye amene ali wamasiye ndithu, nasiyidwa yekha, ayembekezera Mulungu, nakhalabe m'mapembedzo ndi mapemphero usiku ndi usana.

6. Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo,

7. Ndipo izi ulamulire, kuti akhale opanda ciremao

8. Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yace ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lace, wakana cikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupira.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 5