Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 4:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya cikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosoceretsa ndi maphunziro a ziwanda,

2. m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olocedwa m'cikumbu mtima mwao monga ndi citsulo camoto;

3. akuletsa ukwati, osivitsa zakudya zakuti, zimene Mulungu anazilenga kuti acikhulupiriro ndi ozindikira coonadi azilandire ndi ciyamiko.

4. Pakuti colengedwa conse ca Mulungu ncabwino, ndipo palibe kanthu kayenera kutayika, ngati kalandiridwa ndi ciyamiko;

5. pakuti kayeretsedwa ndi Mau a Mulungu ndi kupemphera.

6. Ngati ukumbutsa abale zinthu izi, udzakhala mtumiki wabwino wa Kristu Yesu, woleredwa m'mauwo a cikhulupiriro, ndi malangizo abwino amene udawatsata;

7. koma nkhani zacabe ndi za akazi okalamba ukane. Ndipo udzizoloweretse kucita cipembedzo;

8. pakuti cizolowezi ca thupi cipindula pang'ono, koma cipembedzo cipindula zonse, popeza cikhala nalo Lonjezano la ku moyo uno, ndi la moyo ulinkudza.

9. Okhulupirika mauwa ndi oyenera kulandiridwa konse.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 4