Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 1:6-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pace;

7. pofuna kukhala aphunzitsi a lamulo ngakhale sadziwitsa zimene azmena, kapena azilimbikirazi.

8. Koma mudziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu acita nalo monga mwa lamulo,

9. podziwa ici, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osayeruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ocimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,

10. acigololo, akucita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana naco ciphunzitso colamitsa;

11. monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine.

12. Ndimyamika iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Kristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,

13. ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wacipongwe; komatu anandicitira cifundo, popeza ndinazicita wosazindikira, wosakhulupirira;

14. koma cisomo ca Ambuye wathu cidacurukatu pamodzi ndi cikhulupiriro ndi cikondi ciri mwa Kristu Yesu.

15. Mauwa ali okhulupirika ndi oyenera konse kuti awalandire, kuti Kristu Yesu anadza ku dziko lapansi kupulumutsa ocimwa; wa iwowa ine ndine woposa;

16. komatu mwa ici anandicitira cifundo, kuti mwa ine, woyamba, Yesu Kristu akaonetsere kuleza mtima kwace konse kukhale citsanzo ca kwa iwo adzakhulupirira pa iye m'tsogolo kufikira moyo wosatha.

17. Ndipo kwa Mfumu yosatha, yosabvunda, yosaoneka, Mulungu wa yekha, ukhale ulemu ndi ulemerero, kufikira nthawi za nthawi. Amen.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 1