Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 1:5-11 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. koma citsirizo ca cilamuliro ndico cikondi cocokera mu mtima woyera ndi m'cikumbu mtima cokoma ndi cikhulupiriro cosanyenga;

6. zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pace;

7. pofuna kukhala aphunzitsi a lamulo ngakhale sadziwitsa zimene azmena, kapena azilimbikirazi.

8. Koma mudziwa kuti lamulo ndi labwino, ngati munthu acita nalo monga mwa lamulo,

9. podziwa ici, kuti lamulo siliikika kwa munthu wolungama, koma kwa osayeruzika ndi osamvera lamulo, osapembedza, ndi ocimwa, osalemekeza ndi amnyozo, akupha atate ndi akupha amai, akupha anzao,

10. acigololo, akucita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana naco ciphunzitso colamitsa;

11. monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 1