Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 1:3-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

3. Monga ndinakudandaulira iwe utsalire m'Efeso, popita ine ku Makedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,

4. kapena asasamale nkhani zacabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'cikhulupiriro;

5. koma citsirizo ca cilamuliro ndico cikondi cocokera mu mtima woyera ndi m'cikumbu mtima cokoma ndi cikhulupiriro cosanyenga;

6. zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pace;

7. pofuna kukhala aphunzitsi a lamulo ngakhale sadziwitsa zimene azmena, kapena azilimbikirazi.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 1