Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 1:10-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. acigololo, akucita zoipa ndi amuna, akuba anthu, amabodza, olumbira zonama, ndipo ngati kuli kena kakutsutsana naco ciphunzitso colamitsa;

11. monga mwa Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene anandisungitsa ine.

12. Ndimyamika iye wondipatsa ine mphamvu, ndiye Kristu Yesu, Ambuye wathu, kuti anandiyesa wokhulupirika, nandiika kuutumiki,

13. ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wacipongwe; komatu anandicitira cifundo, popeza ndinazicita wosazindikira, wosakhulupirira;

14. koma cisomo ca Ambuye wathu cidacurukatu pamodzi ndi cikhulupiriro ndi cikondi ciri mwa Kristu Yesu.

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 1