Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Timoteo 1:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. PAULO, mtumwi wa Kristu Yesu monga mwa cilamuliro ca Mulungu Mpulumutsi wathu, ndi ca Kristu Yesu, ciyembekezo cathu:

2. kwa Timoteo mwana wanga weniweni m'cikhulupiriro: Cisomo, cifundo, mtendere za kwa Mulungu Atate ndi kwa Kristu Yesu Ambuye wathu.

3. Monga ndinakudandaulira iwe utsalire m'Efeso, popita ine ku Makedoniya, nditeronso, kuti ukalamulire ena ajawa asaphunzitse kanthu kena,

4. kapena asasamale nkhani zacabe, ndi mawerengedwe osalekeza a mafuko a makolo, ndiwo akuutsa mafunso, osati za udindo wa Mulungu umene uli m'cikhulupiriro;

5. koma citsirizo ca cilamuliro ndico cikondi cocokera mu mtima woyera ndi m'cikumbu mtima cokoma ndi cikhulupiriro cosanyenga;

6. zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pace;

Werengani mutu wathunthu 1 Timoteo 1