Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 4:13-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. koma popeza mulawana ndi Kristu zowawa zace, kondwerani; kutinso pa bvumbulutso la ulemerero wace mukakondwere kwakukurukuru.

14. Mukatonzedwa pa dzina la Kristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.

15. Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wocita zoipa, kapena ngati wodudukira;

16. koma akamva zowawa ngati Mkristu asacite manyazi; koma alemekeze Mulungu m'dzina ili.

17. Cifukwa yafika nthawi kuti ciweruziro ciyambe pa nyumba ya Mulungu; komangati ciyamba ndi ife, citsiriziro ca iwo osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu cidzakhala ciani?

18. Ndipo ngati munthu wolungama apulumuka ndi kuyesetsa kokha kokha, munthu wosapembedza ndi wocimwa adzaoneka kuti?

19. Koteronso iwo akumva zowawa monga mwa cifuniro ca Mulungu aike moyo wao ndi kucita zokoma m'manja a Wolenga wokhulupirika.

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 4