Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 3:11-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. j Ndipo apatuke pacoipa, nacite cabwino;Afunefune mtendere ndi kuulondola.

12. Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama,Ndi makutu ace akumva rembedzo lao;Koma nkhope ya Ambuye iri pa ocita zoipa,

13. Ndipo ndani iye amene adzakucitirani coipa, ngati mucita naco cangu cinthu cabwino?

14. Komatu ngatinso mukamva zowawa cifukwa ca cilungamo, odala inu; ndipo musaope pakuwaopa iwo, kapena musadere nkhawa;

15. koma mumpatulikitse Ambuye Kristu m'mitima yanu; okonzeka nthawi zonse kucita codzikanira pa yense wakukufunsani cifukwa ca ciyembekezo ciri mwa inu, komatu ndi cifatsondi mantha;

16. ndi kukhala naco cikumbu mtima cabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino m'Kristu akacitidwe manyazi.

17. Pakuti, kumva zowawa cifukwa ca kucita zabwino, ndi kumva zowawa cifukwa ca kucita zoipa, nkwabwino kumva zowawa cifukwa ca kucita zabwino, ngati citero cifuniro ca Mulungu,

18. Pakuti Kristunso adamva zowawa kamodzi, cifukwa ca macimo, wolungama m'malo mwa osalungama, kuti akatifikitse kwa Mulungu; wophedwatu m'thupi, koma woparsidwa moyo mumzimu;

19. m'menemonso anapita, nalalikira mizimu inali m'ndende,

20. imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m'masiku a Nowa, pokhala m'kukonzeka cingalawa, m'menemo owerengeka, ndiwo amoyo asanu ndi atatu, anapulumutsidwa mwa madzi;

21. cimenenso cifaniziro cace cikupulumutsani tsopano, ndico ubatizo, kosati kutaya kwa litsiro lace la thupi, komatu funso lace la cikumbu mtima cokoma kwa Mulungu, mwa kuuka kwa Yesu Kristu;

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 3