Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 3:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Momwemonso, akazi inu, mverani amuna anu ainu nokha; kuti, ngatinso ena samvera mau, akakodwe opanda mau mwa mayendedwe a akazi;

2. pakuona mayendedwe anu oyera ndi kuopa kwanu.

3. Amene kukometsera kwanu kusakhale kwa kunja, kuluka tsitsi ndi kubvala za golidi, kapena kubvala cobvala;

4. koma kukhale munthu wobisika wamtima, m'cobvala cosaola ca mzimu wofatsa ndi wacete, ndiwo wa mtengo wace wapatali pamaso pa Mulungu.

5. Pakuti koteronso kale akazi oyera mtima, akuyembekezera Mulungu, anadzikometsera okha, namvera amuna ao a iwo okha;

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 3