20. Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pocimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pocita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapirira, kumeneko ndiko cisomo pa Mulungu.
21. Pakuti kudzacita ici mwaitanidwa; 1 pakutinso Kristu anamva zowawa m'malo mwanu, 2 nakusiyirani citsanzo kuti mnkalondole mapazi ace;
22. 3 amene sanacita cimo, ndipo m'kamwa mwace sicinapezedwa cinyengo;
23. 4 amene pocitidwa cipongwe sanabwezera cipongwe, pakumva zowawa, sanaopsa, koma 5 anapereka mlandu kwa iye woweruza kolungama;
24. 6 amene anasenza macimo athu mwini yekha m'thupi mwace pamtanda, kuti ife, 7 titafa kumacimo, tikakhale ndi moyo kutsata cilungamo; 8 ameneyo mikwingwirima yace munaciritsidwa nayo.
25. Pakuti 9 munalikusocera ngati nkhosa; koma rsopano mwabwera kwa 10 Mbusa ndi Woyang'anira wa moyo wanu.