Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Petro 2:13-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Tadzigonjani kwa zoikika zonse za anthu, cifukwa ca Ambuye; ngakhale kwa mfumu, monga mutu wa onse;

14. kapena kwa akazembe, monga otumidwa ndi iye kukalanga ocira zoipa, koma kusimba ocita zabwino.

15. Pakuti cifuniro ca Mulungu citere, kuti ndi kucita zabwino mukatontholetse cipulukiro ca anthu opusa;

16. monga mfulu, koma osakhala nao ufulu monga cobisira coipa, koma ngati akapolo a Mulungu.

17. Citirani ulemu anthu onse. Kondani abale. Opani Mulungu, Citirani mfumu ulemu.

18. Anyamata inu, gonjerani ambuye anu ndi kuopa konse, osati abwino ndi aulere okha, komanso aukali.

19. Pakuti ici ndi cisomo ngati munthu, cifukwa ca cikumbu mtima pa Mulungu alola zacisoni, pakumva zowawa wosaziyenera.

20. Pakuti mbiri yokoma yanji, mukapirira pocimwa ndi kubwanyulidwapo? Komatu, ngati pocita zabwino, ndi kumvako zowawa mumapirira, kumeneko ndiko cisomo pa Mulungu.

Werengani mutu wathunthu 1 Petro 2