Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Atesalonika 5:16-28 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. Kondwerani nthawi zonse;

17. Pempherani kosaleka;

18. M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.

19. Musazime Mzimuyo;

20. Musanyoze maaenero;

21. Yesani zonse; sungani cokomaco,

22. Mupewe maonekedwe onse a coipa.

23. Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda cirema pa kudza kwace kwa: Ambuye wathu Yesu Kristu.

24. Wakuitana inu ali wokhulupirika, amenensoadzacicita.

25. Abale, z tipempherereni ife.

26. 1 Lankhulani abale onse ndi cipsompsono copatulika.

27. Ndikulumbirirani pa Ambuye kuti 2 kalatayu awerengedwe kwa abale onse.

28. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu Kristu cikhale nanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Atesalonika 5