14. Koma tidandaulira inu abale, yambirirani ampwayi, limbikitsani amantha mtima? cirikizani ofok a, mukhale oleza mtima pa onse.
15. Penyani kuti wina asabwezere coipa womcitira coipa; komatu nthawi zonse mutsatire cokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.
16. Kondwerani nthawi zonse;
17. Pempherani kosaleka;
18. M'zonse yamikani; pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu ca kwa inu, mwa Kristu Yesu.
19. Musazime Mzimuyo;
20. Musanyoze maaenero;
21. Yesani zonse; sungani cokomaco,
22. Mupewe maonekedwe onse a coipa.
23. Ndipo Mulungu wa mtendere yekha ayeretse inu konsekonse; ndipo mzimu wanu ndi moyo wanu ndi thupi lanu zisungidwe zamphumphu, zopanda cirema pa kudza kwace kwa: Ambuye wathu Yesu Kristu.