Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Atesalonika 4:14-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pakuti ngati tikhulupirira kuti Yesu adamwalira, nauka, koteronso Mulungu adzatenga pamodzi ndi iye iwo akugona mwa Yesu.

15. Pakuti ici tinena kwa inu m'mau a Ambuye, kuti ife okhala ndi moyo, otsalira kufikira kufikanso kwa Ambuye, sitidzatsogolera ogonawo.

16. Pakuti Ambuye adzatsika Kumwamba mwini yekha ndi mpfuu, ndi mau a mngelo wamkuru, ndi lipenga la Mulungu; ndipo akufa mwa Ambuye adzayamba kuuka;

17. pamenepo ife okhala ndi moyo, otsalafe, tidzakwatulidwa nao pamodzi m'mitambo, kukakomana ndi Ambuye mumlengalenga, ndipo potero tidzakhala ndi Ambuye nthawi zonse.

18. Comweco, tonthozanani ndi mau awa,

Werengani mutu wathunthu 1 Atesalonika 4