Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Atesalonika 4:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cotsalira tsono, abale, tikupemphani ndi kukudandaulirani mwa Ambuye Yesu, kuti, monga munalandira kwa ife mayendedwe okoma, muyenera kuyendanso ndi kukondweretsa Mulungu, monganso mumayenda, eurukani koposa momwemo.

2. Pakuti mudziwa malangizo amene tinakupatsani mwa Ambuye Yesu.

3. Pakuti ici ndi cifuniro ca Mulungu, ciyeretso canu, kuti mudzipatule kudama;

4. yense wa inu adziwe kukhala naco cotengera cace m'ciyeretso ndi ulemu,

5. kosati m'eiliro ca cilakolako conyansa, monganso amitundu osadziwa Mulungu;

6. asapitirireko munthu, nanyenge mbale wace m'menemo, cifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinacitapo umboni.

7. Pakuti Mulungu sanaitana ife titsate cidetso, koma ciyeretso.

8. Cifukwa cace iye wotaya ici, sataya munthu, komatu Mulungu, wakupatsa Mzimu wace Woyera kwa inu.

9. Koma kunena za cikondano ca pa abale sikufunika kuti akulembereni; pakuti wakukuphunzitsani ndi Mulungu, kuti mukondane wina ndi mnzace;

10. pakutinso munawacitira ici abale onse a m'Makedoniya lonse. Koma tikudandaulirani, abale, mueurukireko koposa,

11. ndi kuti muyesetse kukhala cete ndi kucita za inu eni ndi kugwira nchito ndi manja anu, monga tinakuuzani;

12. kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.

13. Koma sitifuna, abale, kuti mukhale osadziwa za iwo akugona; kuti mungalire monganso otsalawo, amene alibe ciyembekezo.

Werengani mutu wathunthu 1 Atesalonika 4