1. Cifukwa cace, posakhoza kulekereranso, tidabvomereza mtima atisiye tokhaku Atene;
2. ndipo tinatuma Timoteo, mbale wathuyo ndi mtumiki wa Mulungu m'Uthenga Wabwino wa Kristu, kuti akhazikitse inu; ndi kutonthoza inu za cikhulupiriro canu;
3. kuti asasunthike wina ndi zisautso izi, pakuti mudziwa nokha kuti adatiika ife ticite izi.
4. Pakutinso, pamenetinali ndi inu tinakuuziranitu kuti tidzamva zisautso; monga kudacitika, monganso mudziwa.
5. Mwa ici inenso, posalekereranso, ndinatuma kukazindikira cikhulupiriro canu, kuti kaperta: woyesa akadakuyesani, ndipo cibvuto cathu cikadakhala copanda pace.