Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Atesalonika 2:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Komatu tinakhala ofat sa pakati pa inu, monga m'mene mlezi afukata ana ace a iye yekha;

8. kotero ife poliralira inu, tinabvomera mokondwera kupereka kwa inu si Uthenga Wabwino wa Mulungu wokha, komanso moyo wathu, popeza mudakhala okondedwa kwa ife.

9. Pakuti mukumbukila, abale, cigwiritso cathu ndi cibvuto cathu; pocita usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu, tinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu.

10. Inu ndinu mboni, Mulungunso, kuti tinakhala oyera mtima ndi olungama ndi osalakwa kwa inu akukhulupirira;

11. monga mudziwa kuti tinacitira yense wa inu pa yekha, monga atate acitira ana ace a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kucita umboni,

12. kuti muyende koyenera Mulungu, amene akuitanani inu mulowe ufumu wace wa iye yekha, ndi ulemerero.

13. Ndipo mwa icinso ife tiyamika Mulungu kosalekeza, kuti, pakulandira mau a Uthenga wa Mulungu, simunawalandira monga mau a anthu, komatu monga momwe ali ndithu, mau a Mulungu, amenenso acita mwa inuokhulupirira.

14. Pakuti inu, abale, munayamba kukhala akutsanza a Mipingo ya Mulungu yokhala m'Yudeya mwa Kristu Yesu; popeza zomwezi mudazimva kowawa nelinunso pamanja pa a mtundu wanu wa inu nokha, monganso iwowapa manja a Ayuda;

Werengani mutu wathunthu 1 Atesalonika 2