Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Atesalonika 2:16-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

16. natiletsa ife kuti tisalankhule ndi akunja kuti apulumutsidwe; kudzaza macimo ao nthawi zonse; koma mkwiyo wafika pa iwo kufikira cimariziro.

17. Koma ife, abale, angakhale adaticotsa kusiyana nanu kanthawi, osapenyana maso, koma kusiyana mtima ai, tinayesetsa koposa kuona nkhope yanu ndi cilakolako cacikuru;

18. cifukwa tinafuna kudza kwa inu, inedi Paulo ndatero kamodzi kapena kawiri; koma Satana anatiletsa.

19. Pakuti ciyembekezo cathu, kapena cimwemwe, kapena korona wakudzitamandira naye nciani? si ndinu nanga pamaso pa Ambuye wathu Yesu m'kufika kwace?

20. Pakuti inu ndinu ulemerero wathu ndi cimwemwe cathu.

Werengani mutu wathunthu 1 Atesalonika 2