Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 9:20-23 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

20. Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;

21. kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo twa Kristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.

22. Kwa ofoka ndinakhala ngati wofoka, kuti ndipindule ofoka, Ndakhala zonse kwa anthu onse, 1 kuti pali ponse ndikapulumutse ena.

23. Koma ndicita zonse zifukwa ca Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 9