Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 9:17-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Pakuti ngati ndicita ici cibvomerere, mphotho ndiri nayo; koma ngati si cibvomerere; anandikhulupirira m'udindo.

18. Mphotho yanga nciani tsono? Kuti pakulalikira Uthenga Wabwino ndiyese Uthenga Wabwino ukhale waulere, kuti ndisaipse ulamuliro wanga wa mu Uthenga Wabwino.

19. Pakuti pokhala ndinali mfulu kwa onse, ndinadzilowetsa ndekha ukapolo kwa onse, kuti ndipindule ocuruka.

20. Ndipo kwa Ayuda ndinakhala monga Myuda, kuti ndipindule Ayuda; kwa iwo omvera lamulo monga womvera lamulo, ngakhale sindinakhala ndekha womvera lamulo, kuti ndipindule iwo omvera malamulo;

21. kwa iwo opanda lamulo monga wopanda lamulo, wosati wakukhala ine wopanda lamulo kwa Mulungu, koma womvera lamulo twa Kristu kuti ndipindule iwo opanda lamulo.

22. Kwa ofoka ndinakhala ngati wofoka, kuti ndipindule ofoka, Ndakhala zonse kwa anthu onse, 1 kuti pali ponse ndikapulumutse ena.

23. Koma ndicita zonse zifukwa ca Uthenga Wabwino, kuti ndikakhale woyanjana nao.

24. Kodi umudztwa kuti iwo akucita makani a Iwiro, athamangadi onse, koma nmodzi alandira mfupo? Motero 2 thamangani, kuti mukalandire.

25. Koma yense wakuyesetsana adzikaniza zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakubvunda; 3 koma ife wosabvunda.

26. Cifukwa cace ine ndithamanga cotero, si nonga cosinkhasinkha. Ndilimbaaa cotero, si monga ngati kupanda nlengalenga;

27. koma 4 ndipumpuatha thupi langa, ndipo ndiliyesa capolo; kuti, kapena ngakhale rdalalikira kwa ena, 5 ndingakhale votayika ndekha.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 9