Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 7:7-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Koma mwenzi anthu onse akadakhala monga momwe ndiri ine ndekha. Koma munthu yense ali nayo mphatso yace ya iye yekha kwa Mulungu, wina cakuti, wina cakuti.

8. Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli bwino kwa iwo ngati akhala monganso ine.

9. Koma ngati sadziwa kudziletsa, akwatitsidwe; pakuti nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.

10. Koma okwatitsidwawo ndiwalamulira, si ine ai, koma Ambuye, kuti mkazi asasiye mwamuna,

11. komanso ngati amsiya akhale osakwatiwa, kapena ayanjanitsidwenso ndi mwamunayo, ndipo mwamuna asalekane naye mkazi.

12. Koma kwa otsalawo ndinena ine, si Ambuye, Ngati mbale wina ali naye mkaziwosakhulupira, ndipo iye abvomera mtima kukhala naye pamodzi, asalekane naye.

13. Ndipo mkazi amene ali naye mwamuna wosakhulupira, nabvomera mtima iye kukhala naye pamodzi, asalekane naye mwamunayo.

14. Pakuti mwamuna wosakhulupirayo ayeretsedwa mwa mkaziyo, ndi mkazi wosakhulupira ayeretsedwa mwa mbaleyo; ngati sikukadatero, ana anu akadakhala osakonzeka, koma tsopano akhala oyera.

15. Koma ngati wosakhulupirayo acoka, acoke. M'mirandu yotere samangidwa ukapolo mbaleyo, kapena mlongoyo, Koma Mulungu watiitana ife mumtendere.

16. Pakuti udziwa bwanji mkazi iwe, ngati udzapulumutsa mwamunayo? kapena udziwa bwanji, mwamuna iwe, ngati udzapulumutsa mkazi?

17. Koma, monga Ambuye wagawira kwa yense, monga Mulungu waitana yense, momwemo ayende. Ndipo kotero ndiika m'Mipingo yonse.

18. Kodi waitanidwa wina wodulidwa? Asakhale wosadulidwa. Kodi waitanidwa wina wosadulidwa? Asadulidwe.

19. Mdulidwe ulibe kanthu, ndi kusadulidwa kulibe kanthu, koma kusunga kwa malamulo a Mulungu.

20. Yense akhale m'maitanidwe m'mene anaitanidwamo.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 7