Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 7:26-32 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

26. Cifukwa cace ndiyesa kuti ici ndi cokoma cifukwa ca cibvuto ca nyengo yino, kuti nkwabwino kwa munthu kukhala monga ali.

27. Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.

28. Koma ungakhale ukwatira, sunacimwa; ndipo ngati namwali akwatiwa, sanacimwa. Koma otere adzakhala naco cisautso m'thupi, ndipo ndikulekani.

29. Koma ici nditi, abale, yafupika nthawi, kuti tsopano iwo akukhala nao akazi akhalebe monga ngati alibe;

30. ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu;

31. ndi iwo akucita nalo dziko lapansi, monga ngati osacititsa; pakuti maonekedwe a dziko ili apita.

32. Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 7