Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 6:8-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Koma muipsa, nimunyenga, ndipo mutero nao abale anu.

9. Kapenasimudziwa kuti osalungama sadzalandira ufumu wa Mulungu? Musasoceretsedwe; adama, kapena opembedza mafano, kapena acigololo, kapena olobodoka ndi zoipa, kapena akudziipsa ndi amuna,

10. kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

11. Ndipo ena ainu munali otere; koma munasambitsidwa, koma munayeretsedwa, koma munayesedwa olungama, m'dzina la Ambuye Yesu Kristu, ndi mwa Mzimu wa Mulungu wathu.

12. Zinthu zonse ziloledwa kwa ine; koma si zonse zipindula, Zinthu zonse ziloledwa kwa ine, koma sindidzalamulidwa naco cimodzi.

13. Zakudya ndizo za mimba, ndi mimba ndiyo ya zakudya; koma Mulungu adzathera iyi ndi izi. Koma thupi siliri la cigololo, koma la Ambuye, ndi Ambuye wa thupi;

14. koma Mulungu anaukitsa Ambuye, ndiponso adzaukitsa ife mwa mphamvu yace.

15. Kodi simudziwa kuti matupi anu ali ziwalo za Kristu? cifukwa cace ndidzatenga ziwalo za Kristu kodi, ndi kuziyesa ziwalo za mkazi waciwerewere? Msatero iai.

16. Kapena simudziwa kuti iye wophatikidwa ndi mkazi waciwerewere ali thupi limodzi? Pakuti, awiriwo, ati, adzakhala thupi limodzi.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 6