Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 6:17-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

17. Koma iye wophatikidwa ndi Ambuye ali mzimu umodzi.

18. Thawani dama. Cimo liri lonse munthu akalicita liri kunja kwa thupi; koma waciwerewere acimwira thupi lace la iye yekha.

19. Kapena simudziwa kuti thupi lanu liri kacisi wa Mzimu Woyera, amene ali mwa inu, amene muli naye kwa Mulungu? Ndipo simukhala a inu nokha.

20. Pakuti munagulidwa ndi mtengo wace wapatali; cifukwa cace lemekezani Mulungu m'thupi lanu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 6