Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 6:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kodiakhoza winawa inu, pamene ali nao mlandu pa mnzace, kupita kukaweruzidwa kwa osalungama, osati kwa oyera mtima?

2. Kapena kodi simudziwa kuti oyera mtima adzaweruza dziko lapansi? Ndipo ngati dziko lapansi liweruzidwa ndi inu, muli osayenera kodi kuweruza timilandu tocepacepa?

3. Kodi simudziwa kuti tidzaweruza angelo? koposa kotani nanga zinthu za moyo uno?

4. Cifukwa cace, ngati muli nayo mirandu ya zinthu za moyo uno, kodi muweruzitsa iwo amene ayesedwa acabe mu Mpingo?

5. Ndinena ici kukucititsani inu manyazi. Kodi nkutero kuti mwa inu palibe mmodzi wanzeru, amene adzakhoza kuweruza pa abale,

6. koma mbale anena mlandu ndi mbale, ndikotu kwa osakhulupira?

7. Koma pamenepo pali cosowa konse konse mwa inu, kuti muli nayo mirandu wina ndi mnzace. Cifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? simusankhula cifukwa ninji kulolakunyengedwa?

8. Koma muipsa, nimunyenga, ndipo mutero nao abale anu.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 6