Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 5:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Kwamveka ndithu kuti kuli cigololo pakati pa inu, ndipo cigololo cotere conga sicimveka mwa amitundu, kuti wina ali naye mkazi wa atate wace.

2. Ndipo mukhala odzitukumula, kosati makamaka mwacita cisoni, kuti acotsedwe pakati pa inu iye amene anacita nchito iyi.

3. Pakuti inedi, thupi langa kulibe, koma mzimu wanga ulipo, ndaweruza kale, monga ngati ndiripo,

4. m'dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,

5. kumpereka iye wocita cotere kwa Satana, kuti lionongeke thupi, kuti mzimu upulumutsidwe m'tsiku la Ambuye Yesu.

6. Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti cotupitsa pang'ono citupitsa mtanda wonse?

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 5