Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 3:5-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

5. Ndipo Apolo nciani, ndi Paulo nciani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.

6. Ndinanka ine, anathirira Apolo; kama Mulungu anakulitsa.

7. Cotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; kama Mulungu amene akulitsa.

8. Koma wookayo ndi wothirirayoali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yace ya iye yekha, monga mwa kucititsa kwace kwa iye yekha.

9. Pakuti ife ndife anchito anzace a Mulungu; cilimo ca Mulungu, cimango ca Mulungu ndi inu.

10. Monga mwa cisomo ca Mulungu cidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo.

11. Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu.

12. Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala va mtengo wace, mtengo, maudzu, dziputu,

13. nchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, cifukwa kuti yabvumbuluka m'moto; ndipo mota wokha udzayesera nchito ya yense ikhala yotani.

14. Ngati nchito ya munthu ali yense khala imene anaimangako, adzaandira mphotho.

15. Ngati nchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zace; koma iye yekha adzapulumutsilwa; koma monga momwe mwa noto.

16. Kodi simudziwa kuti muli Kacisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

17. Ngati wina aononga kacisi wa Mulungu, ameneyo Mulungu adzamuononga; pakuti kacisi wa Mulungu ali wopatulika, ameneyo ndi inu.

18. Munthu asadzinyenge yekha; igati winaayesa kuti ali wanzeru nwa inu m'nthawi yino ya pansi iano, akhale wopusa, kuti akakhale vanzeru.

19. Pakuti nzeru ya dziko ina lapansi iri yopusa kwa Mulungu, Pakuti, kwalembedwa, iye agwira mzeru m'cenjerero lao;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 3