Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 3:1-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ine, abale, sindinakhoza kulankhula ndi inu manga ndi auzimu, koma monga athupi, monga makanda mwa Kristu.

2. Ndinaiyetsa inu mkaka, si cakudya colimba ai; pakuti simunaeikhoza; ngakhale tsopano lino simucikhoza; pakuti mulinso athupi;

3. pakuti, pokhala pali nkhwidzi ndi ndeu pakati pa inu simuli athupi kodi, ndi kuyendayenda monga mwa munthu?

4. Pakuti pamene wina anena, ine ndine wa Paulo; koma mnzace, Ndine wa Apolo; simuli anthu kodi?

5. Ndipo Apolo nciani, ndi Paulo nciani? Atumiki amene munakhulupirira mwa iwo, yense monga Ambuye anampatsa.

6. Ndinanka ine, anathirira Apolo; kama Mulungu anakulitsa.

7. Cotero sali kanthu kapena wookayo, kapena wothirirayo; kama Mulungu amene akulitsa.

8. Koma wookayo ndi wothirirayoali amodzi; koma yense adzalandira mphotho yace ya iye yekha, monga mwa kucititsa kwace kwa iye yekha.

9. Pakuti ife ndife anchito anzace a Mulungu; cilimo ca Mulungu, cimango ca Mulungu ndi inu.

10. Monga mwa cisomo ca Mulungu cidapatsidwa kwa ine, ngati mwini mamangidwe waluso, ndinaika maziko, koma wina amangapo. Koma yense ayang'anire umo amangira pamenepo.

11. Pakuti palibe munthu akhoza kuika maziko ena, koma amene aikidwako, ndiwo Yesu Kristu.

12. Koma ngati wina amanga pa mazikowo, golidi, siliva, miyala va mtengo wace, mtengo, maudzu, dziputu,

13. nchito ya yense idzaonetsedwa; pakuti tsikulo lidzaisonyeza, cifukwa kuti yabvumbuluka m'moto; ndipo mota wokha udzayesera nchito ya yense ikhala yotani.

14. Ngati nchito ya munthu ali yense khala imene anaimangako, adzaandira mphotho.

15. Ngati nchito ya wina itenthedwa, zidzaonongeka zace; koma iye yekha adzapulumutsilwa; koma monga momwe mwa noto.

16. Kodi simudziwa kuti muli Kacisi wa Mulungu, ndi kuti Mzimu wa Mulungu agonera mwa inu?

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 3