Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 2:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo ine, abale, m'mene ndinadza kwa inu, sindinadza ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu cinsinsi ca Mulungu.

2. Pakuti ndinatsimikiza mtima kuti ndisadziwe kanthu mwa inu koma Yesu Kristu, ndi iye wopacikidwa.

3. Ndipo ine ndinakhala nanu mofoka ndi m'mantha, ndi monthunthumira mwambiri.

4. Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau okopa a nzeru, koma m'cionetso ca Mzimu ndi ca mphamvu;

5. kuti cikhulupiriro canu cisakhale m'nzeru ya anthu, koma mu mphamvu ya Mulungu.

6. Koma tilankhula nzeru mwa angwiro; koma si nzeru ya nthawi yino ya pansi pano, kapena ya akulu a nthawi yino ya pansi pano, amene alinkuthedwa;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 2