Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 16:19-24 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

19. Mipingo ya ku Asiya ilankhula inu. Akulankhulani ndithu inu mwa Ambuye, Akula ndi Priska, pamodzi ndi Mpingo wa m'nyumba yao,

20. Akulankhulani inu abale onse. Lankhulanani ndi kupsompsona kopatulika.

21. Kulankhula kwa ine Paulo ndi dzanja langa.

22. Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.

23. Cisomo ca Ambuye Yesu Kristu cikhale ndi inu.

24. Cikondi canga cikhale ndi inu nonse mwa Kristu Yesu. Amen.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 16