Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 16:11-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. cifukwa cace munthu asampeputse, Koma mumperekeze mumtendere, kuti akadze: kwa ine; pakuti ndimuyembekezera pamodzi ndi abale,

12. Koma za Apolo, mbaleyo, ndamuumiriza iye, adze kwa inu pamodzi ndi abale; ndipo sicinali cifuniro cace kuti adze tsopano, koma adzafika pameneaona nthawi.

13. Dikirani, cirimikani m'cikhulupiriro; dzikhalitseni amuna, limbikani.

14. Zanu zonse zicitike m'cikondi.

15. Koma ndikupemphani inu, abale, (mudziwa banja la Stefana, kuti ali cipatsocoundukula ca Akaya, ndi kuti anadziika okha kutumikira oyera mtima),

16. kuti inunso mubvomere otere, ndi yense wakucita nao, ndi kugwiritsa nchito.

17. Koma ndikondwera pa kudza kwao kwa Stefana, ndi Fortunato, ndi Akayiko; cifukwa iwo anandikwaniritsa cotsalira canu.

18. Pakuti anatsitsimutsa mzimu wanga ndi wanu; cifukwa cace muzindikire otere.

19. Mipingo ya ku Asiya ilankhula inu. Akulankhulani ndithu inu mwa Ambuye, Akula ndi Priska, pamodzi ndi Mpingo wa m'nyumba yao,

20. Akulankhulani inu abale onse. Lankhulanani ndi kupsompsona kopatulika.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 16