Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 16:1-5 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma za copereka ca kwa oyera mtima, mongandinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero citani inunso.

2. Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha; monga momwe anapindula, kuti zopereka zisacitike pakudza ine.

3. Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.

4. Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.

5. Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Makedoniya; pakuti ndidzapyola Makedoniya;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 16