Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 16:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Koma za copereka ca kwa oyera mtima, mongandinalangiza Mipingo ya ku Galatiya, motero citani inunso.

2. Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha; monga momwe anapindula, kuti zopereka zisacitike pakudza ine.

3. Ndipo pamene ndifika, ndidzatuma iwo amene mudzawayesa oyenera, ndi akalata, apite nayo mphatso yanu ku Yerusalemu.

4. Ndipo ngati kuyenera kwa ine kupitanso, adzapita nane.

5. Koma ndidzadza kwa inu, nditapyola Makedoniya; pakuti ndidzapyola Makedoniya;

6. ndipo kapena ndidzakhalitsa ndi inu, kapenanso kugonera nyengo yacisanu kuti mukandiperekeze ine kumene kuli konse ndipitako,

7. Pakuti sindifuna kukuonani tsopano popitirira; pakuti ndiyembekeza kukhala ndi inu nthawi, ngati alola Ambuye.

8. Koma ndidzakhaia ku Efeso kufikira Penteskoste,

9. Pakuti panditsegukira pa khomo lalikuru ndi locititsa, ndipo oletsana nafe ndi ambiri.

10. Koma akadza Timoteo, penyani kuti akhale ndi inu wopanda mantha; pakuti agwira nchito ya Ambuye, monganso ine;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 16