Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 15:8-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. ndipo potsiriza pace pa onse, anaoneka kwa inenso monga mtayo.

9. Pakuti ine ndiri wamng'ono wa atumwi, ndine wosayenera kuchedwa mtumwi, popeza ndinalondalonda Eklesia wa Mulungu.

10. Koma ndi cisomo ca Mulungu ndiri ine amene ndiri; ndipo cisomo cace ca kwa ine sicinakhala copanda pace, koma ndinagwirira nchito yocuruka ya iwo onse; koma si ine, komacisomo ca Mulungu cakukhala ndi ine.

11. Ngati ine tsono, kapena iwowa, kotero tilalikira, ndi kotero munakhulupira.

12. Koma ngati Kristu alalikidwa kuti waukitsidwa kwa akufa, nanga ena mwa inu anena bwanjikuti kulibe kuuka kwa akufa?

13. Koma ngati kulibe kuuka kwa akufa, Kristunso sanaukitsidwa;

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 15