Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

1 Akorinto 15:53-58 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

53. Pakuti cobvunda ici ciyenera kubvala cisabvundi, ndi 19 caimfa ici kubvala cosafa.

54. Ndipo pamene cobvunda ici cikadzabvala cisabvundi ndi caimfa ici cikadzabvala cosafa, pamenepo padzacitika mau olembedwa, 20 Imfayo yamezedwa m'cigonjetso.

55. 21 Imfawe, cigonjetso cako ciri kuti? Imfawe, mbola yako iri kuti?

56. Koma mbola ya imfa ndiyo ucimo; koma 22 mphamvu ya ucimo ndiyo cilamulo:

57. koma 23 ayamikike Mulungu, amene atipatsa ife cigonjetso mwa Ambuye wathu Yesu Kristu.

58. Cifukwa cace, abale anga okondedwa, 24 khalani okhazikika, osasunthika, akucuruka mu ncbitoya Ambuye, nthawi zonse, podziwa kuti kucititsa kwanu sikuli cabe mwa Ambuye.

Werengani mutu wathunthu 1 Akorinto 15